28/07/2026
ZOMBA NDI MULANJE: 3.7MW YAIWALIKA YOMWE INGATHETSE MDIMA π²πΌπ‘
Anzanga, munanenapo kuti "bwanji magetsi akuchepa?"
YANKHO: Sitikusowa magetsi. Tikusowa nzeru.
MBIRI YOBISIKA YA MALAWI:
1. ZOMBA PLATEAU HYDRO β 1950s
Pa Mulunguzi River. Kukula: 1.2MW
Inapereka magetsi ku Zomba Town YONSE kwa zaka 40.
INATSEKEDWA 1998. Lero ndi mabwinja.
Mtengo okonza: K3.5 BILLION yokha.
2. RUO HYDRO β MULANJE, RUGERI TEA ESTATE β 1930s
Pa Ruo River, phazi la Phiri la Mulanje. Kukula: 2.5MW
Inapereka magetsi ku factory ya tiyi kwa zaka 70.
INAYIMA 2005. Lero ndi mabwinja.
Mtengo okonza: K5.25 BILLION yokha.
ZONSE: 1.2MW + 2.5MW = 3.7MW YAIWALIKA
MTENGO OKONZA ZONSE: K8.75 BILLION YOKHA
3.7MW = Magetsi a nyumba 3,700 KWAULERE
KOMA BOMA LIKUFUNA CHIYANI?
K40.5 BILLION PAMWEZI kwa zaka 15 = K7.29 TRILLION
Kuti lipeze 50MW yatsopano.
MASAMU A CHOONADI:
Kukonza zakale: K2.36 Billion pa MW imodzi
Kumanga zatsopano: K145.8 Billion pa MW imodzi
MAGETSI AKALE NDI OTSIKA MTENGO 62x
NZERU ZATSOPANO: DAMU LIMODZI, PHINDU LITATU
Madzi otuluka mu turbine sawonongeka. Nde bwanji osawagwiritsanso?
NDONDOMEKO YA ZOMBA MULTI-PURPOSE = K6 BILLION:
1. K3.5B β Bwezerani 1.2MW magetsi
2. K1.5B β Yeretsani madzi β Anthu 50,000 amwa madzi aukhondo
3. K1B β Irrigation β Ma hectare 500 alime chaka chonse
PHINDU: MAGETSI + MADZI + CHAKUDYA ndi K6B yokha
RUO HYDRO ANGACHITE CHOMWECHO KU MULANJE:
2.5MW magetsi + Madzi + Ulimi wa tiyi = K7.5B
FUNSO LALIKULU:
Chifukwa chani tikutaya K960 MILLION chaka chilichonse kugula magetsi
pamene K5.25B ikanathetsa vuto kwamuyaya?
Chifukwa chani Zomba ili mumdima zaka 28
pamene turbine ili chabe pa Mulunguzi?
YANKHO:
1. ESCOM safuna mpikisano. Akufuna nonse mugule kwa iwo.
2. Andale amakonda ma project a K7 Trillion kuti adye ma Billion.
3. Palibe chifuniro chothandiza Zomba ndi Mulanje.
IS IT FAIR?
Mwana wobadwa ku Zomba 1998 lero ali ndi zaka 28.
Sanawonepo magetsi odalirika. Koma akulipira K9,000 pa unit. Pamwezi
ZAKA 28 ZA MDIMA ZOKWANIRA