Verdant Agrifarms & suppliers

Verdant Agrifarms & suppliers we also aim at teaching farmers how to become successful in livestock production.

verdant Agrifarms is a farm located in lunzu Blantyre that produces and supplies livestock products like fertilized eggs, chicks and chickens, ducks, pigeons, pigs and more.

Kodi ichi chili pa zingati mbali za kwanuko Kuno anyamata apa kameza roundabout simomwe atidabwitsira ndi mitengo yawo e...
12/08/2026

Kodi ichi chili pa zingati mbali za kwanuko
Kuno anyamata apa kameza roundabout simomwe atidabwitsira ndi mitengo yawo eeh

Tiwetadi koma nkhunda zimenezo inu

KADYETSEREDWE KOYENERA KA NKHUKU ZA MAZIRA Ambili mumadziwa kuti nkhuku za mazira timazidyetsera kawili pa tsiku. Njira ...
12/08/2026

KADYETSEREDWE KOYENERA KA NKHUKU ZA MAZIRA

Ambili mumadziwa kuti nkhuku za mazira timazidyetsera kawili pa tsiku. Njira imeneyi ili ndi ubwino wake komabe lelo tufuna tikuuzeni kanthu kena kobisika ka kadyetseredwe kabwino.

Nkhuku za mazira zimafunika pogawa chakudya chake muzichulutsa chakudya Cha mmawa. ndekuti Cha madzulo chizikhala chocheperako. Tikutamthauza kuti ngati nkhuku zanu zimadya 10kgs patsiku muzipereka 6kgs mmawa kenako 4 kgs madzulo (60/40% rule).

Chifukwa chiyani zimafunika kutero??

Nkhuku zimafunika chakudya chochulukilapo mmawa kuti zikhale ndi mphanvu zambili zothamangila komanso zogwilitsa ntchito pa tsiku limenelo. Zimafunikanso zigwilitse ntchito chakudya china poyamba kupanga egg York ( ka mkati mwa dzira ka yellow 🟡) komanso kuti zipange choyera Cha dzira, mkati mwa tsiku lomwelo. Zimenezi zimafunika 60% ya chakudya Cha nkhuku.

Masana kutatsala maola pakati pa 4 ndi 6 zisanalowe mu mdima zimafunika ziphakenso kapena kulandila chakudya china chotsala chija 40%. Chakudyachi chimayenera kukhala chocheperako chifukwa nkhukuzo sizifuna mphanvu zambili sinanga zikhala zikugona. Komabe popeza usiku ndi Nthawi imene zimapanga egg shell ( chigoba Cha dzira ) zimafunika zigwilitse ntchito chakudyachi mpaka mpaka itamaliza kupanga dzira lomwe limadzaikiridwa mawa lakelo. Chifukwa dongosolo limeneli limachotsa mphanvu zina, mmawa wa tsiku linalo imadzafunika kudya chochulukilapo imene ndi 60% ija.

Inu mumagwilitsa ntchito luso liti podyetsa nkhuku zanu??
Tiphunzire nawo luso lanu

Verdantagrifarms
Lunzu Blantyre

Si kale kwambili pamene takumana ndi kudziwana pamudzi pano koma tapanga ubale. Komanso mwatilemekeza inu ndipo zambili ...
12/08/2026

Si kale kwambili pamene takumana ndi kudziwana pamudzi pano koma tapanga ubale. Komanso mwatilemekeza inu ndipo zambili zachitika. ife mau athu ndi othokoza aliyense wapamudzi pano pothandiza verdantagrifarms kufika apa.

Maso athu akulunjikabe popereka upangiri wabwino, kupereka poyambila pabwino Kwa amene akufuna kuyamba ndi kuthandiza oyamba kale komanso kupitiliza kupanga supply mwa dongosolo ma livestock products athu.

We might be far from the target but we also very far from where we started so let's celebrate every achievement of this journey. Long live verdantagrifarms lunzu Blantyre.

KODI MUYENERA KUGULA MA FEEDERS NDIMA DRINKER ANGATI KUTI AKWANIRE NKHUKU ZANU??Funso ili limabalalitsa kwambili anthu n...
12/08/2026

KODI MUYENERA KUGULA MA FEEDERS NDIMA DRINKER ANGATI KUTI AKWANIRE NKHUKU ZANU??

Funso ili limabalalitsa kwambili anthu ndipo tingati ndi lovutilapo ndithu Kuti anthu ambili aliyankhe mwa chindunji. Ngakhale ife anamanyonyolo sitiyankha wachidule.

Chifukwa chiyani tikutero?? Ma feeder ndima drinkers alipo a mitundu yambili ndipo amakhala ndi ma design osiyanasiyananso kuphatikiza pamenepo amakhala ndi kukula Kosiyanasiyana. Monga taonetsera mu ma pictures mmusi.

Si zokhazo chiwerengero chama feeder ndima drinker chimasiyananso potengera size ya nkhuku zimene zikuwetedwa komanso mtundu WA nkhukuzo.

Choncho kuti munthu alandile yankho la chindunji amafunika kufotokoza Kaye mtundu WA feeder imene akuganiza zogula, size kapena kuchuluka Kwa chakudya kapena madzi amene feeder kapena drinker yo imanyamula, amafunika kuchulanso size ndi mtundu wa NKHUKU zimene akufuna kuweta. Zikatere timayankhana mosavuta.

Mutakhala inu mungayankhe bwanji funso limeneli???
Tiuzeni tikopere

Verdantagrifarms
Lunzu Blantyre

KODI UYENERA KUYAMBA NDI NDALAMA ZINGATI ULIMI WA NKHUKU?? KODI UYENERA KUYAMBA NDI NKHUKU ZINGATI KUTI ZIYENDE BWINO.Fu...
12/08/2026

KODI UYENERA KUYAMBA NDI NDALAMA ZINGATI ULIMI WA NKHUKU?? KODI UYENERA KUYAMBA NDI NKHUKU ZINGATI KUTI ZIYENDE BWINO.

Funso limene timafunsidwa kwambili. Kodi verdantagrifarms imayankha kuti chani??

Ulimi wa nkhuku ulibe capitolo yachikhalire kapena chiwerengero chokhazikika Cha nkhuku zoyambira. Iyi ndi business imene imayambila paliponse mogwirizana ndi kuthekera kwanu. Munthu amayamba ulimi umenewu potengera zimene Ali nazo. Zinthu ndi ndalama zimene muli nazo ndi zomwe zimanena kuti muyambe ndi zochuluka bwanji.

Capitolo yanu imagawidwa mu zinthu zosiyanasiyana monga ma feeders, drinkers, khola, katemera, feed yokwanira ndi zina zambili (fixed inputs) zomwe mlimi aliyense amayenera kukhala nazo. Ndalama ina yotsalayo ndi imene imapereka chiwerengero Cha nkhuku zoyenera kuyamba nazo.

Ngati muli ndi kuthekera kwakukulu, mumathanso kungoganiza kuti muyambe ndi nkhuku zochuluka bwanji kenako mumadziwa kuchuluka Kwa zomwe mungalowetse zomwe ndima fixed inputs.

Kodi mutakhala inu mungayankhe bwanji funso limeneli?! Tiuzeni tibwere style yanu

Zili ndiinu kudzagula mazira a mbewu ndi kupeza nawo upangiri wa ulele wa ulimi umenewu ndi kapangidwe ka chakudya pompo...
11/08/2026

Zili ndiinu kudzagula mazira a mbewu ndi kupeza nawo upangiri wa ulele wa ulimi umenewu ndi kapangidwe ka chakudya pompoponpo.
Zilinso ndi inu kuyamba ulimi wa nkhuku koma ndi nkhuku zokongola za pure pofika ku verdantagrifarms. Zilitu ndi inu kukana zonsezi ndi kungotolapo mazira pamene mwafikapo koma osapeza zonsezi

Verdant Agrifarms
Lunzu Blantyre

Mu parent stock yathu munali adha awa  eeeh akulu amenewa ntchito ankagwira kwambili kaya ankadya chani kaya koma ma tha...
11/08/2026

Mu parent stock yathu munali adha awa eeeh akulu amenewa ntchito ankagwira kwambili kaya ankadya chani kaya koma ma thadzi ena mpaka kumamuthawatu.

Ngakhale kuti ankagwira ntchito bwino koma color yake mukhosi lake inkaononga mbewu. Anapiye amabadwatu ndi ma colors kudabwa kuti imeneyi mikolongwe koma 😂😂

Tinachiona Cha nzeru kumuchotsamo kuti color ikhare ya black yokha. Inu mukuona kuti tinachita bwino?? Kapena popeza ndi dolo timubwezere

11/08/2026

DZIWANI UBWINO WA ULIMI WA BAKHA PART 2
Osamangoti abakha ndi anyansi iyayi tiyeni tiweteko abakha

GROWING FARMERS SCALING FARMS Week ino verdantagrifarms ikupereka upangiri wa ulele ndi MAZIRA a mbewu a ulele Kwa anthu...
10/08/2026

GROWING FARMERS SCALING FARMS

Week ino verdantagrifarms ikupereka upangiri wa ulele ndi MAZIRA a mbewu a ulele Kwa anthu awili awa
Khwiyawoh Precious Chimtengo Jnr
Wedson Dickson
Big congratulations to these new farmers in town to be created by poultry masters verdantagrifarms.

Anthu 8 otsatilawa anayesesetsa ndipo Ali mu top 10 ya week ino. Iwowa alandila ma 2pin a bundle lelo lisanathe. Amene atchulidwe mmusimu, popanga comment musaiwale kuika number ya Airtel money ndi dzina lake zikomo. CHONDE ku WhatsApp inbox kukuyenera kubwera amene awina mazira enafe tiyeni tingolemba ma number athu tigule bundle

1. Zex Panje 5675 pts
2. VD Makunganya 5674 pts
3. Francisco M. Chimwaza 4970 pts
4 Alepha Malunga 4942 pts
5 Mphatso Muliya 4767 pts
6 Ackim Mataka 678 pts
7 Salim Kachingwe 542 pts
8 Inno Rosicky Ngoleka 470 pts

Once again congratulations 👏 to our 2 winners we wish you the best and big up to top 10 yonse ntchito mwaigwila. Tikumanenso mu program yomwei Monday likubwerali zikomo

Verdantagrifarms
LUNZU BLANTYRE

Kodi abale achina chawinga achina faith ndi rose sangafuneko mazira a fertilized kapena ma chicks kkkk Ifetu tikhoza kut...
10/08/2026

Kodi abale achina chawinga achina faith ndi rose sangafuneko mazira a fertilized kapena ma chicks kkkk
Ifetu tikhoza kuthamanga nawo mazira, ma chicks ndi upangiri pa airport atafuna or atati ma point of laying a parent stock koma basi nanga angalime iwowa??

Anyway akulu akulu team iyi ikutinvetsa kukoma mpaka dzulo brooding siinayende fukwa Cha team imeneyi ai amatha kwambili

Congratulations scorchers

Verdantagrifarms
Lunzu Blantyre

Address

Lunzu
Blantyre

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Verdant Agrifarms & suppliers posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share

Category