Wexi ov God

Wexi ov God Zochitika mmasiku omaliza. Anthu okonda ndalama, zosangalatsa, osavera akuwabala, ouma mtima, odzikundikira

15/05/2025

KODI MWADZUDZULIDWA KANGATI...?

📖 MIYAMBO 29:1 "Yemwe aumitsa nkhosi atadzudzulidwa kwambiri, adzasweka modzidzimuka, palibe chomchiritsa"

Choyamba ndimafuna ndi kuuzeni kuti mau oti "KUDZUDZULIDWA" amatathauzo "Kumuuza Mzako Kuti Asiye Mankhalidwe Oyipa Omwe Angamubweretsere Mavuto Mzakoyo,"

Muyenera kuzindikila kuti CHIKONDI ndi chimene chimamupangitsa munthu kuti "afike pomudzudzula mzake yemwe akuchita makhalidwe oipa omwe angamubweretsere mzake ochita zoipayo mavuto"

📖 Chibvumbulutso 3:19 "Onse amene ndiwakonda, NDIWADZUDZULA ndi kuwalanga; potero chita changu, nutembenuke mtima"

Pa 📖 Chibvumbulutso 3:19 tikupeza kuti, MULUNGU anthu amene amawakonda AMAWADZUDZULA kuti asiye uchimo, ndipo chomwe chikumupangitsa MULUNGU kuti afike pomudzudzula munthu ndi chifukwa chakuti MULUNGU amakhala wawoona zowawa ndi zowoopsa zomwe munthuyo adzakumane nazo akadzaponyedwa ku Gahena.

Ndithu MULUNGU chifukwa chomukondetsetsa munthu, nthawi zonse IYE akamuona munthu akuchimwa MULUNGU amachita changu kumudzudzula muthu wochimwayo pofuna kuti asiye uchimowo ndicholinga chakuti munthu ochimwayo asakapezeke ku Gahena.

📖 Miyambo 29:1 "Yemwe aumitsa nkhosi atadzudzulidwa kwambiri, adzasweka modzidzimuka, palibe chomupulumutsa"

Baibulo pa 📖 Miyambo 29:1 likuwulura chisisi chakuti "MUNTHU OCHIMWA AMENE ADZUDZULIDWA MAULENDO OCHULUKA KOMA OSAFUNA KULAPA, ZOTSATILA ZAKE ZIMAKHALA MUNTHU OCHIMWAYU KUPONYEDWA KU GAHENA"

Mfuso Mkumati "Kodi ndi chifukwa chiyani anthu omwe alandira chidzudzulo maulendo ochuluka zedi, zotsatila zake zimakhala anthu otere kuponyedwa ku Gahena...?

YANKHO LIKUPEZEKA PA 📖 AROMA 1:28

📖 Aroma 1:28 Ndipo monga iwo anakana kukhala naye MULUNGU m'chidziwitso chawo, anawapereka MULUNGU KU MTIMA WOKANIKA..."

Abale tandivetserani mwa uzimu pa mfundo yakuti "Anawapereka(Anthu Ochimwa) Ku Mtima Wokanika" 📖 Aroma 1:28,...✍️✍️

MULUNGU akamudzudzula muthu ochimwa maulendo ochuluka, ndipo MULUNGU akaona kuti muthu ochimwayu sakusiyabe makhalidwe onyasa

06/05/2025

Kumapemphera a Malawi 🇲🇼

06/02/2025

Kumapemphera mu nchoonadi Mulungu alipo
Amayi, abambo, mnyamata, mtsikana tayamba tsiku lililonse ndi pemphero kuti nyengo zisinthe koma pakupemphera ndikumukweza Mulungu osaiwala kugwira ntchito molimbikira chifukwa amapatsa olimbikira

Udzadya thukuta lako

Amen

06/02/2025

Muli bwanji a Malawi anzanga.
Lero pa 6 feb 2025 Mulungu wamphanvu zonse watipatsaso moyo waulele. Koma ngakhale izi zili chonchi anthu sitikumulambirabe ambuye wathu tili kakaka kulambira milungu yooneka ndi maso.

Tamvani izi:
Padali mudzi wina ndipo mmudzimo mudali banja lina lomwe amayi pabanjalo ndi amene amakonda kupemphera. Koma kupemphera kwawo kunali ndendende mmene anthu masiku ano tikupempherera. Mayiyo amapemphera mongofuna kumaveka mmudzimo kuti amapemphera, amapanga zachifundo kuthandiza ovutika koma moonetsera koma nkuti panthawiyi anali asanalandire mbuye Yesu mumtima mwake.

Mayiyu masiku ambiri akamapita ku tchalitchi amafusa amusa amuna ake kuti chifukwa chiyani iwowo samapemphera nawo ayi ndipo iwo tsiku lililonse amamuyankha kuti "tonsefe sitinayambe kupempheratu ayi" ndipo iye amakhala odabwa komabe sanasiye kupemphera kwabodzako kufikira pamene tsiku lina lomwe kunachitika zodabwitsa.

Tsiku limeneli abambo aja anaganiza zomuyesa mkazi wake ngati amapempheradi mu nchoona ndipo bambo uja anatsazika kuti akupita ntauni ya mdera lakwawolo mayi uja osadziwa maganizo a amuna akewo.

Ndipo patadzutsa mphindi makumi atatu(30) panaveka odi pakhomo pa mayiyo mai uja atatuluka anadabwa kuti ndikankhalamba kakamuna ndipo kankhalambako kadamuuza mai uja kuti chonde ndithandizeni chakudya njala yandivuta zedi. Koma mai uja adakana nanena kuti iye alibe ufa ayi koma nkhalamba ija idakakamirabe kuti chonde thandizeni koma mayi uja sadasinthe maganizo ayi.
Atakangana ndithu kwa mphindi zingapo nkhalamba ija idachotsa zovala zomwe idavala zija mpamene mayi uja adadzidzimuka kuona kuti adali amuna ake aja kenako abambo aja adamuuza kuti paja ndakhala ndikukuuza kuti tonse munyumba muno sitidayambe kupemphera ndipo mayi uja adadziguguda pa chifuwa ndipo bambo uja adapitiliza nkunena kuti anthu ambiri timapanga zinthu zopemphera kaya zachifundo pofuna kudzionetsa kugulu ngati olungama zomwe ambirife tikupanga koma dziwani kuti simukunamiza munthu koma nokha
Amen

27/01/2025

Moni abale anga tiyeni tilape machimo athu nkuyamba kumutumikira Mulungu wathu wakumwamba.
Nthawi yatha zizindikiro zikuoneka monga nkhondo, kudana mtundu ndi mtundu, kukonda ndalama ndi zina zotero.

Lero m'bale wanga Mulungu wakupatsa moyo waulele pachifukwa ichi tatiye tiyambe kumupembedza chifukwa ndi Mulungu yekha amene ayenera kulambiridwa

Chivumbulutso 13
Amen

Mukhale ndi tsiku lopambana

24/01/2025

Okondedwa abale anga apa ulendo, yambani tsiku lililonnse ndi pemphero kumuthokoza Mulungu potipatsa moyo wa ulele,chifukwa anzathu anafuna akanafika lero naliwonaso dzuwa la lero koma alephera koma pamene iwe waliona uchitenge chinthu cha mtengo wapatali. Anthu kunja kuno akuvutika muzipatala ndi nthenda zosiyanasiyana pamene iwe mphanvu uli nazo koma osakumbuka kumuyamika ambuye Mulungu wamphanvu zonse. Koma dziwani kuti tikamapemphera osaiwala kulimbikira ntchito zathu zosiyanasiyana pakuti ananena kale kuti udzadya thukuta lako.... Amen
Mlaliki 1:1-3

08/01/2025

Muli bwanji anzanga apaulendo?
Lero tikambeko za masiku omaliza ano pankhani yokhudza kupembedza mafano. Masiku omaliza ano anthu ambiri tikupembedza mafano mu njira zosiyanasiyana monga kukonda zamakono,kugwadira mafano eni eniwo, makamaka ma Church ena akuchita kuonetsera koma anthufe osazindikira kuti tikupembedza mafano. Langizo langa ndilakuti chokaniko kumafano amenewo yambani kumutsata Yesu lero. Sankhani Yesu lero kukhala mbuye ndi mpulumutsi wa moyo wako. Amen
Ambuye akudalitseni

07/01/2025

Muli bwanji abale anga apaulendo? Anthu tikamagona nkumadzuka ndimoyo timangozitenga mwachizolowezi koma kunena zoona kudzuka ndi moyo ndi chisomo chopambana komanso chaulele chomwe ambuye Mulungu wathu amationetsera tsiku ndi tsiku. Abale anga tiyeni tizipemphera nthawi yatha zinthu zambiri zikuchitika mwachitsanzo anthu muzipatala akuzunzika mdi nthenda zosiyana siyana, mndende anthu akukumana ndi zovuta koopsa plus kunzuzika koopsa. Tatiyeni tizipemphera komanso kulimbikira kugwira ntchito chifukwa Mulungu wakumwamba sakonda wamanja lende ayi. Khalani olombikira mu zonse ambuye akudalitseni... Amen

04/01/2025

Okondedwa anzanga apaulendo lero pa 4 January 2025 zindikira kuti pofika mu tsiku la lero ambuye atikondera. Tinali nawo abale, tinali nawo anzathu, tinali nawo abwezi omvana nawo koma lero kulibe koma pomwe iwe ndine tili ndi moyo tatiye tipange chisankho choyamba kumutumikira ambuye. Tatiyeni tisiye zina zonse zachikunja timazikonda zija tiyeni tisankhe Yesu mkhristu kukhala mbuye ndi mpulumutsi wa moyo wathu lero. Ambuye akhale nanu! Mlaliki 1 v1-3
Amen

Address

24
Lilongwe

Telephone

+265884929170

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Wexi ov God posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share

Category