Chima TV

Chima TV Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Chima TV, Grocers, Rumphi, Mzuzu.

Ngozi ya ndege yomwe yinachitika ku south korea 22 hours ago now yapha anthu 179 ndipo 2 apulumuka. Ndegeyo yathera pomp...
05/01/2025

Ngozi ya ndege yomwe yinachitika ku south korea 22 hours ago now yapha anthu 179 ndipo 2 apulumuka. Ndegeyo yathera pompo ndi moto waukali koma chodabwitsa BLACK BOX anyamula akupita nayo. FUNSO WHY MALAWI ????

26/12/2024

yathu ya Lero.

Ife a Malawi Eyes Online, sitikudabwa ndi pang'ono pomwe ndi zomwe Anthu maka otsatira chipani cha MCP, akuchita ponyoza ndi kutukwana Bishop wamkulu wa mpingo wa akatolika, Luke Thomas Msusa, kamba kogwilitsa ntchito ufulu wake ofotokoza maganizo ake posagwilizana ndi zotsatira za kafuku fuku wa ngozi ya ndege yomwe inapha Dr Saulosi Chilima ndi Anthu ena asanu ndi atatu (8) ku chikangawa pa 10th June.

Ife a Malawi Eyes Online, tikukumbutsa mtundu mtundu wa Amalawi, kuti Anthu otsatira chipani cha MCP, anatengera khalidwe la Akulu akulu a chipanicho, omwe ankakambirana zofuna kupha ma Bishop a mpingo wa akatolika, kamba koti iwo analemba kalata yodzudzura nkhanza za chipani cha MCP, pansi pano utsogoleri wa Kamuzu Banda, mchaka cha 1992.

"Abwere kuno ma Bishop amenewa ndipo ine ndiwakodzera, anatero Mayi Hilda Manjankhosi, yemwe anali wapambando wa Amayi m'boma la Lilongwe.

"Ndipo lero lomwe lino ma Bishop amenewa afe ndithu dzuwa lisanalowe' anatero Tuzija Phiri, yemwe anali wapambando wa chipani cha MCP, m'boma la kasungu.

Koma bwanji tisaphe ma Bishop amenewa, koma tikumane nawo ndikuchita zokambirana' anatero Kapichita Musa, yemwe anali wapambando wa chipani cha MCP, m'boma la Mangochi.

Aaaaaaaa! Kodi munthu akanyoza Bambo ake umakambirana naye? anafunsa motero Wadson Deleza, yemwe anali nduna ya Boma.

Ayiiiiij timangopha basi, Akulu akulu akale nse a chipani cha MCP pa mkumanowo anayankha motero...

Lero lomwe lino dzuwa lisanalowe ma Bishop amenewa akaoname ndi Mulungu wawo, anagwilizana motero kuti ma Bishop onse aphedwe chifukwa cha kalata yodzudzura nkhanza za Boma, lomwe analemba pa 8th March mchaka cha 1992.
Ngati sitikudabwa ndi kutukwanidwa komanso kunyongedwa kwa Bishop Thomas Luke Msusa, umboni ulipo kuti chipani chawo cha MCP chomwe chinkafuna kupha ma Bishop a mpingo wa akatolika.
Kuti mutipeze mwachangu ndipo mudzimva nkhani zochitika pa Dziko lonse lapansi kuphatikizapo nkhani za nkhondo. Copied from MW eyes online

26/12/2024

Bishop wamkulu wa mpingo wa akatolika m'dziko la Democratic Republic of Congo (DCR) mu akidayosizi ya Kinshasa, Bishop Frindolin Ambogo, wadzudzura Boma la Dzikolo, kamba kolephera kuthanda ndi nkhondo yomwe yakhala ikusautsa nzika za Dzikolo, maka ku chigawo chaku'mawa kwa Dzikolo.

Poyankhula mu uthenga wake wa nyengo ya Khilisimasi kwa nkhosa za chauta za mpingowo, Bishop Frindolin Ambogo, anapitiliza kudzudzura Boma la Dzikolo, kamba ka umphawi omwe wafika povuta kwambiri pakati pa nzika za Dzikolo.

Bishop Frindolin Ambogo, wakhala akudzudzura utsogoleri wa Felix Tshisekedi, yemwe ndi mtsogoleri wa Dzikolo, ndipo kumayambiliro a chaka chino, mlangizi wa Boma la Dzikolo pa nkhani za malamulo, anatsekulira mlandu Bishop Frindolin, ponena kuti anayankhula mau ofuna kudzetsa mpungwe pungwe m'dzikolo.

Izitu zachitika ku Dziko la Democratic Republic of Congo (DRC) pamene kuno kwathu Bishop wamkulu wa mpingowu Thomas Luke Msusa, wati sakukhutitsidwa ndi zotsatira za kafuku fuku wa ngozi ya ndege yomwe inapha Dr Saulosi Chilima ndi Anthu ena asanu ndi atatu (8) ku nkhalango ya chikangawa.

Ndipo pa Dziko lonse lapansi, Mabishop a mpingo wa akatolika, samaopa, samanyengelera, koma kuyankhula chilungamo chokha chokha pa momwe zinthu ziliri m'miko awo.

Kuti inu mutipeze mwachangu ndipo mudzimva nkhani zochitika pa Dziko lonse lapansi kuphatikizapo nkhani za nkhondo, Thinikizani Mau awa ๐Ÿ‘‰ Malawi Eyes Online

Olemba Grant Elisha.

15/12/2024

Let's us gather and think about the natural calamity called CHIDO cyclone

14/12/2024

Lero mesa tisiya kukamba za ndege Donier 228

06/12/2024

Gender Based Violence, DMI-St john the baptist university ๐ŸŽ“ Lilongwe cumpas, meeting today ๐Ÿ‘ฎ ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ”ฅ Must stop it

04/12/2024

Pamene tikuyenda kutolera data ya anthu okonda za chikhalidwe ku Lilongwe ndinafika kumudzi wina mdera la mfumu yayikulu Nsandula komwe ndinapeza anthu akunyadira chikhalidwe chawo motere ๐Ÿ‘‡

04/12/2024

Pamene tikuyenda kutolera data ya anthu okonda za chikhalidwe ndinafika kumudzi wina mdera la Lilongwe mdela la a mfumu yayikulu Nsandula komwe ndinapeza anthu akunyadira chikhalidwe chawo motere๐Ÿ‘‡๐Ÿ‘‡

Address

Rumphi
Mzuzu

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Chima TV posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share

Category