03/07/2025
Osewera wa timu ya Liverpool Diogo Jota wamwalira pa ngozi yagalimoto,
Katswiri wa dziko la Portugal, Jota, yemwe anali ndi zaka 28 zakubadwa pamodzi ndi m'chimwene wake Andre Silva amwalira pa ngoziyi, yomwe idachitika m'chigawo cha Zamora m'dziko la Spain.
Andre Silva, yemwe anali ndi zaka 26 analinso katswiri wosewera mpira, ndi timu yaku Portugal ya Penafiel.
Malinga ndi nyumba youlutsa mawu ya BBC, Jota ndi mchimwene wake adamwalira cha m'ma 00:30 Lachinayi.
Iwo ati galimoto yawo ya Lamborghini, idasiya msewu chifukwa cha kuphulika kwa matayala pomwe idadutsa galimoto ina kenako idayaka moto.
Jota anakwatira Rute Cardoso yemwe anali naye kwa nthawi yaitali, yemwe anali ndi ana atatu, mwezi watha.
Jota adathandizira Liverpool kupambana chikho cha Premier League sizoni yapitayi komanso adaseweranso Portugal pomwe adamenya