Simiyon super stories

Simiyon super stories Cholinga chathu ndikusangalatsa, kudziwitsa komaso kuphuzitsa

pangani follow page

WhatsApp

number 0893035000

06/11/2025

Boma timafuna lija ndilimeneri, kuchotsa M'busa nkuyikapo_____? 😳🇲🇼

04/11/2025

Nyengo zakezi ndikwamwayi ngati tizagulepo galimoto 😥

01/11/2025

Shout out to my newest followers! Excited to have you onboard! Kúlīnjî Mw, Hetherwick Jonas, Luth Makupete, KG Grivin, Francis Banda, Chicco Chiba Bandah

20/10/2025

Big shout out to my newest top fans! Tamie Chilembwe, Brandinah Jere, Carolyn Stafford, Grace Phiri, Memori Banda, Jimmy Mbatata, Dorothy Chaponda, Stanley Chandida, Gerard Thom Chikwakwa, Mervice Banda, Stewart Victor Newa, Sallomy Rabson, Zione Mwale, Alinafe Baibe, Mphatso kaipa, Samfray MW, Luwiza Edison, LaJabu Ssamu, Linly Mathiya, Tasleem William, Qüãvø Killß Jeke, Brenda Kamanga, Achilandanda Rajabuh, ۦٰٰٰٰٰٰۦٰٰٰٰٰٰ ۦٰٰٰٰٰٰۦٰٰٰٰٰٰ ۦٰٰٰٰٰٰۦٰٰٰٰٰٰ ۦٰٰٰٰٰٰۦٰٰٰٰٰٰ, Squecy Kate, Penuel Nyozani, Henry, Queen Sheera Somanje, Princess Mwanza, Aggie Aggie, Sumiyat Sadiyat, Kelita Pidoo Maluwa, Alex E Mical, Yvonne Trust, Agness Sandram, Jayne Lackson, Angellah Chiwayu, Wanangwa Banda, Maggie Tizola, Florence Khoza, Ireen Mphande, Daniel Kapuza Bvumbwe, Meya Tembo, ۦٰٰٰٰٰٰۦٰٰٰٰٰٰ ۦٰٰٰٰٰٰۦٰٰٰٰٰٰ ۦٰٰٰٰٰٰۦٰٰٰٰٰٰ ۦٰٰٰٰٰٰۦٰٰٰٰٰٰ, Justine Mwase Mazon, Thomas Dymon July, Mçløúd Bûtâwø, Grace Mhango, Henry Mlauzi, Doreen Mackphat

04/10/2025

🔰 PALIBE CHOSATHA 🔰

PART 5

Written by simiyon mwale

Wosayiwala kupanga follow page ya Simiyon super stories k*ti zambiri zisamakuphonyeni ....

Tamala atangofika anaphana maso ndi Madam aja amene anali atangoyima pamalo pena pamene anali akugwiritsa ntchito Ana ena ndipo Madam aja anamukodola Tamala amene sanachedwe koma kupita k*ti akave zimene akumuyitanila....

Atafika madam aja anayamba avekele..
"Wadzuka bwanji Tamala?
" Ndadzuka bwino Kay inuyo Madam?
"Ineso Ndadzuka bwino, aaa lero ndiri ndizochitika zina Ku School kuno kubwela alendo ndimati ukangoweluka ukandikozeleko chakudya kunyumba. Komano ngati kwanuko kuli ntchito yoti ukagwire palibe vuto ukhoza kupita ndek*ti ndiwona k*ti nditani.
" Aa wosadandaula madam ndikapanga zimene mwandiuzazo ndikangoweluka.
"Chabwino ndakuva basi ndizomwezi ukhoza nkumapita. Aaaa mayesotu atsala pang'ono ndiye kumawelenga
" Eya tiziwelenga".Atangotelo Tamala anachokapo pamalo paja ndikumapita kumene kunali anzake.

Atangofika anamupeza nzake Tapiwa akunsesa ndipo atangomuwona nzakeyu apatu anayamba kulankhula Ali...
"Haa! inuyo ameneyo!, eee azathutu mwayaka moto pasukulu pano. Mamawa wokha wuno mpaka anyamata awiri Mmm ndisaname sisi ndinu mbamba.
" Heey! Tapiwa ukukamba zichani kodi? Mose wayambira kundipopako ndapanga chani ine?"
"K*k ukufuna k*thawamo chani?, Ukulankhula ngati sukukudziwa chimene ndik*tanthauza bwanji, Wosandibalaritsa ine bola ndanena k*ti inuyo ndi 1 chifukwa kanyamata koyela kaja nde kari srs2 ak*ti ukaweluka akufuna atakumana nawe".Atangotelo Tapiwa apatu Tamala anawoneka wodabwa ndipo analiponya fuso avekele...

"Tapiwa? Uk*tanthawuza chani kodi? Ndisaname nkhani zakozo zikundibalaritsa wanva. Ukukamba za M'nyamata watani? ko komaso ndi ndani nyamata ukumunenayo nanga akundifuna k*ti ndatani ineyo?"
"K*k m'tsikana moti sukumudziwa Alick?, Ndi Alick amene amandiuza zimenezo bola ndakuwuza ine ngati simunakumanepo kuyambira tsopano ukhale ukudziwa zimenezo k*ti popita apanga za iweyo k*kk". Analankhula uku akuseka Tapiwa ndipo panthawiyi Tamala sanayankhe koposa kungotenga kachikwama kake k**akope nkumapita panzele chifukwa belu linari litalira.

Mafuso wopanda mayankho anali akuzungulira mutu mwantsikanayu ndipo anali wobalarika kwambiri ndizinene anamuuza nzake uja. Atakhala panzele paja chilichose chinayenda monga mwanthawi zonse kenako atamaliza aliyese anakalowa munkalasi imene amaphuzila. Munkalasi mene amaphuzila Tamala muja munalowa M'phuzitsi wina amene anatenga phuzilo lake ndipo anaphuzitsa mpakana anamaliza.

Nthawi ya yopumulira inakwana apatu Tamala anatuluka pamodzi ndi nzake uja ndipo anapita kukakhala pamalo Pena popita mphepo uku makope ndi mabuku awo alimanja. Atakhala pamalo paja kenako anayamba kuwelenga

" Bro mwakawona?. Kakuchita kuwara ngati katsika kuchokela kumwamba amwene, Eee ndisaname Namadingo sananame Kumalawi kuno ngenge zilikodi. Tangomuwona nkhope yakeyo ndisaname Kumwetulila kwake kukupangitsa ntima wanga kugunda ndithu"
"K*k bro mukamba ziti kodi?
" Ndukambatu zachiphadzuwa man"
"Aaaa man chiphadzuwa chake chitiso ?
" Woo tiziti wayamba khungu? moti pantengopo sukuwonapo atsikana awiri?"
"Ndikuwawona ndiye pali chiphadzuwa pamenepo?"
"K*k man nangova k*ti dzinalake ndi Tamala eee ndisaname bro nkazi amemeyu mulungu anadekhapo ndithu". Anatelo mwana wamamuna uyutu anali Alick kulankhula uku dzanja lake atagwila kuchigama kwake kumene tindevu tidali titangoyamba kumene kumera.

" K*k Man ndikuwona ngati mutu wanu wasiya kugwira ntchito ndithu"
"Bwanjiso man?
" Iweyo ukuwonaso wekha nkaziyo mene akuwonekela. Zikuchita kuwonetselatu k*ti amagona munchisakasa ameneyu. Iweyo kwanu ndikophura kugwira nkazi ameneyu anthu akhoza kumak*tenga ngati wamisala ndisakunamize M'kulu ukuyenera kuganiza bho. Tangomutaye nkazi ameneyo uyang'ane nkazi wina woti angak*thandize wosati nyasi ukukambazo wanva k*k".analankhula nzake wa Alick uja uyutu anali Jose.

"Mmm bro kulankhula kwabwanji kumeneko? Umphawi wakwawoyo sungapangitse kuchotsa chikondi chimene ndirinacho paiyeyo. Ndisakubisileni man nkazi ameneyo ndiyesa mwayi moti ndamufotokozelapo kale nzake uja k*ti popita ndikumana naya. ukudzi chani?, panopa ndikudziwa akulingalira za ine pamene alipo".Analankhula motelo m'nyamata uku akumuyang'anitsitsa ntsikanayo amene panthawiyi anali busy maso ake pa kope kuri kuwelenga.
🔥🔥🔥

KUMBUKILANI KUYIKA COMMENT YANU MUKAMALIZA KUWELENGA.

MACOMMEMT AKUTI NEXT, UMAKWANA, ILIBHO, AMANDIGWWTSA ULESI CHONDE IKANI COMMENT YACHILIMBIKITSO NGATI MUKUWELENGA

🙏🙏🙏🙏
Nthawi inari ikupita mwapang'ono pang'ono ndipo kukamba za Aphiri ndi akazi awo anali Akuweluka pamunda paja k*tengela k*ti dzuwa rinali litatentha.
" Apatu tizipita mukuwona bwanji?"
"" Zoonadi kandime katsalaka tizamaliza madzulo wano, ngati Tamala sabwerelaso Ku School mwina azatithandizila".Anambewe anayankhila uku ak*tenga khasu lawo kupatsa amuna awo chifukwa iwe amafuna atoleko tinkhuni.

Ananyamuka wose Aphiri ananyamura Makasu awiri pamene akazi awo Anambewe anali ataseza tinkhuni. Ulendo unali uk*theka uku tinkhaniso tikuvumba moti anangozindikila afika kunyumba. koma atangofika anayima Kaye koma modabwa atawona Chitseko chanyumba yawo ndichotsekula.

Apatu anayang'anizana ndipo aliyese anali akuzifusa mafuso muntima mwaka amene samawatulutsa ndipo amasowa mayankha. anayang'ana dzuwa Aphiri anawona k*ti iyi sinthawi imene Ana awo amabwelera kuchokela Ku sukulu.

IKUPITILIRABE....

Pangani share nkhaniyi kuma group ena k*ti azanuso awelenge nawo💥🔥 ipatseni moto ndima like komaso ma comment anu 💥

😀😂 Kwachematu Kwachema, Alick kuyipatsa moto, k*k Jose nayeso AAA kusokoneza k*kk ine 😅 Kodi kunyumba mwalowa ndani? ine ndiri pheee pano kudikila part yotsatila.

💓💃💃💃
inuyo chofunika ndikupanga like komaso share kuma group ena k*ti nkhaniyi azanuso awelenge nawo 🔥💥 titipatse moto

wosayiwala kuyika Comment yanu ndimene imandipatsa chilimbikitso k*ti ndizipitiliza kulemba nkhani 🔥💥 yayamba kununkhilatu 😂

wosayiwala kupanga follow page ya simiyon super stories k*ti nkhaniyi isamakuphonyeni

simiyon super stories

= kusangalatsa
= kudziwitsa
= kuphuzitsa
ndicho cholinga changa ✔

03/10/2025

🔰 PALIBE CHOSATHA 🔰

PART 4

Written by simiyon mwale

Wosayiwala kupanga follow page ya Simiyon super stories k*ti zambiri zisamakuphonyeni ....

Tamala ndi Amayi ake aja anafika pakhomo paja uku awose ataseza madzi. atatula apatu Anambewe anawayitana amuna awo ndipo sanakhalitse koma anabwela. Tamala analipompo ndipo amayi aja anamuyang'ana Tamala ndipo bambo aja anayamba kulankhula avekele....

"Mwandiyitana pamenepo basi mukungoyang'anana ine ndiziti chani? tandiuzeni zimene mukufuna kunenazo ndikufuna ndikaguleko Bhonya ine nkamwamu khambi".Analankhula bambo aja uku akukoza koza chisapato chawo chimene chinari chakuda.

"Tamalayu ndikuchoka kudambo anandiwuza k*ti.... apatu mayi aja anafotokoza chilichose chimene chinachitika kusukulu izitu zinali zimene anawafotokozela Tamala ndipo Aphiri atava zankhaniyi sanalankhure koposa kungodzuka nkumapita kunsika. Apatu mayi aja anamuyang'anaso mwana wawo kenako analankhula avekele...
" Wosadandaula sik*ti akukwiyira ayi ndikamba nawo akabwelako. Tapita ukatsuke mbale kunja kukuda uku". Anatelo anambewe uku ak*tenga kachiseso nkumakozako pakhomo.

Nthawi inari ikupita mwapang'ono pang'ono ndipo kukamba za Aphiri anayenda zachangu mpaka anafika kunsika kuja. Atafika analowa mu shop ndikugula mafuta wophikila kenako anatuluka ndikupita kumene amagulitsilako nsomba. Atafika kumeneko anayang'ana pamene panali nsomba zabwino ndipo atazipeza anagula.

Kam'dima kanali katagwa ndithu ndipo mwezi ndiwumene unayamba kugwila ntchito k*ti kunja kuziwala. Aphiri ananyamuka nkumabwelera kunyumba uku akuyimba kalikhweru kuli kusangalalira ndiwo zimene anagulazo chifukwa iyi inali ngati nyama yawo. Kukamba mosabwisa anthuwa amakumana nazo moyowu amawuva kuwawa osati masewela moti nthawi zambiri Aphiri akakhala amalingalira kwambiri za Ana awo aja chifukwa nde anali anzelu osati masewela.

Chimene chimawadetsa nkhawa kwambiri inari ndalama ya school fz ndipo apa ndipamene amalingalirapo kwambiri. Komabe amangozilimbitsa ntima k*ti azaziwona k*tsogolo.

Ulendo unari uk*theka wopita kunyumba ndipo alimkati moyenda anava kumbuyo ngati kukubwela munthu ndipo sanapilire koma kuchewuka ndipo atangocheuka anangondikila nchenga uli kumaso k*ti azikuwa mbama inawafikanso ndipo anagwa pansi.

Apatu anthu aja Anatola nsomba zija mwachangu changu ndipo wina anapisa munthumba ndik*tengamo kandalama kamene kanatsalako kunsika kuja. Apatu anathawa ndikuwasiya Aphiri akulimbana ndi nchenga umene unari utadzadza kumaso. zinawatengela nthawi k*ti ayambe kuwona bwino bwino ndipo atamaliza kuchotsa apatu anadzuka nkumapita kunyumba uku akupukusa mutu wopanda nyanga kuli kuzivela chisoni.

Anayenda zachangu m'paka anafika kunyumba kuja ndipo atangofika analunjika kuchipinda kwawo zimene zinawadabwitsaso akazi awo ndipo sanaugwile m'tima koma kuwatsatira amuna awowo aja. Atafika Kuchipinda kuja anawapeza amuna awo akupuputa nkhope yawo ndichinsalu ndipo akazi awo aja atawona k*ti ndiwo sizikuwoneka komaso ndimene amawonekela amuna awo panthawiyi analiponya n
mfuso avekele...

"Bambo chachitika ndi chani?, kodi mumathamanga ndiye munagwa?
" Eee amake Tamala, Kaya nditsoka kaya ndiminyama ndisaname sindikuvetsetsa.
"Bwanjiso bambo?, kapena munakuna ndi afisi?
" Afisi? Mmm ayi ndithu ngati ndi afisi afisi ake ndi anthu. Ndinagula chilichose bwino bwino koma ndikubwelako chapakadambo paja ndinangovatu ngati kumbuyo kukubwela munthu ndipo pamene ndimati ndizicheuka nangozindikila nchenga wandifika kumaso".Apatu Aphiri anafotokoza chilichose chimene chinachitika. Ndipo akazi awo atangova zimenezo anagwetsa nkhope yawo pansi kuli kuwavela chisoni amuna awo.

"Ndiye mwati ndalamafo akubelani?
" Eyaka nditangogwa ndipamene wina amapitsa muthuma ndik*tenga ndalama moti ndik**akhala k*ti ndinatenga kafoni kangaka bwezi pano ndikukamba k*ti kapota ndithu.
"Pepani tithokoze k*ti sanakuvulazeni kwambiri.
" Zoonadi.
"Nsimatu ndinaphikilatu moti ndimadikira ndiwozo.
" Aaa bas nanga titani tangophikani nfutsa bola tilume basi".Anatelo Aphiri aja kuwawuza akazi awo.

Mosakharitsa akazi awo aja anakatenga mfutsa ndikukaphika, ataphika anatenga chakudyacho ndikupititsa pabalaza pamene amadyela. Anayitana Benja amene anali kuchipinda kwake kumene amajambura tianthu mumadziwa zochitika za Ana. Kenako wose anasonkhana pabalaza paja ndikuyamba kudya wose ngati banja.

🙏🙏🙏🙏

kumbukilani kuyika comment yachilimbikitso muk**aliza kuwelenga dziwani k*ti ma comment woti Next, Ina ,umakwana, amandigwetsa ulesi. Tiyeni tiyipatse moto 🔥💥

🙏🙏🙏🙏

Nthawi inari ikupita pang'ono pang'ono ndipo atamaliza kudya aliyese analita kuchipinda kukagona. Ndipo Tamala Atafika kuchipinda kwake kuja anagwila makope ake asanayambe kugona anawelengapo kwakanthawi kochepa ngati mene amachitila nthawi zonse. Atawelengapo kwakanthawi kenako anagona

Kumamba za Aphiri ndi akazi awo anali akulingarila za kuganyu kukacha ndipo anagona mwatchelu. Atambala monga mwanthawi zonse analira ndipo Aphiri chak*tulo tulo anava ndipo anazindikira k*ti kunja kwacha. Apatu anawadzutsa akazi awo aja kenako wose anatenga makasu ulendo wakuganyu kuja.

Mosakhalitsa anafika kunyumba kwa m'ponda makwacha kuja ndipo Atafika pa geti anagogoda ndipo mulonda anatsekula. Chokha chongowawona anawauza k*ti alowe kenako mulonda kuja anatsekaso kenako iye anathamanga ndikukadziwitsa abwana ake aja. Atawawuza abwana aja abwanawo anawuza anyamata awo k*ti akawadulire ndime Aphiri aja ndipo Aphiri ndi akazi awo aja pamodzi ndi anyamata aja anatengana ulendo wakumunda.

Atafika chilichose chinayenda mwadongosolo moti Aphiri ndi akazi awo aja anayamba kulimba ndipo anyamata aja anabwelela kunyumba. Aphiri nde kunali kuponya khasu wosati masewela moti anafika paja povulira malaya kusonyeza k*ti ntchito inari itafika pamponda chimela.

Dzuwa linari likukwela ndithu moti kukamba za ana aja anali atanyamuka ulendo wakusukulu monga mwanthawi zonse. Tamala atangofika anaphana maso ndi Madam aja amene anali atangoyima pamalo pena pamene anali akugwiritsa ntchito Ana ena ndipo Madam aja anamukodola Tamala amene sanachedwe koma kupita k*ti akave zimene akumuyitanila....

IKUPITILIRABE....

Pangani share nkhaniyi kuma group ena k*ti azanuso awelenge nawo💥🔥 ipatseni moto ndima like komaso ma comment anu 💥

😀😂 Kwachema 😅 Bhonya sanadyedwe, Ndalama zalita k*k anthu vipongwe 😂 Kodi Tamala awuzidwa zotani ndi madam ake? one ndiriphe kudikila part yotsatila.
💓💃💃💃
inuyo chofunika ndikupanga like komaso share kuma group ena k*ti nkhaniyi azanuso awelenge nawo 🔥💥 titipatse moto

wosayiwala kuyika Comment yanu ndimene imandipatsa chilimbikitso k*ti ndizipitiliza kulemba nkhani 🔥💥 yayamba kununkhilatu 😂

wosayiwala kupanga follow page ya simiyon super stories k*ti nkhaniyi isamakuphonyeni

simiyon super stories

= kusangalatsa
= kudziwitsa
= kuphuzitsa
ndicho cholinga changa ✔

02/10/2025

🔰 PALIBE CHOSATHA 🔰

PART 3

Written by simiyon mwale

Wosayiwala kupanga follow page ya Simiyon super stories k*ti zambiri zisamakuphonyeni ....

Benja anafika pamene panali makolo akewa ndipo Mr Phiri sanachedwe koma kulivumbulutsa fuso avekele....

"heey Benja kusangalara kumeneko tiziti kusukulu kuneneko kunali chani?, komaso tiziti njara sikukuwawa?". anawaponya mafuso awiri aphiri uku akumugwila padzanja mwana wawo.
" Mmm ayiso Ababa kungoti panopa njara sikundiwawa koma pamene tinali munkalasi ndipamene njara imandiwawa mpaka ndinagona.
"Sikukuwawa? wadya chani usakhaletu unathawira iwe nkumakawenkheza". awa Ali a mayi ake nawoso kulankhula koma modadwa.
" Heey Benja tafotokoza unali k*ti? unalidi kusukulu iwe?
"Eya ababa Ku Ku kungoti"
"kungoti chani? talankhula zoveka apa ndisanakukwapule unali k*ti". analankhula bambo aka koma mowopseza zimene zinapangitsa mwanayu kugwidwa mantha

anakhala chete mwana uja uku akunjenjemera chifukwa chamantha. amaganiza k*ti akanena mwina bambo take akhoza kumumenya chifukwa ndimene amawonekela panthawiyi anali atadzadzidwiratu ndi nkwiyo.

" Mwawonatu anambewe zija ndimanena nthawi zonse k*ti mwana uyu masikuwano anayamba zibwana. pano kusukulu sakukhalako akumangokhalira makomo mwa anthu kumapemphetsa. Mwana ameneyu ndamenene Kufuna kuwononga mbiri yanga basis anthu aziti ndikukanika kulela mwana zoona.

Muzikhala nawo Pasi Ana anuwa uphawi uli lakhomo pano chisakhale chipsinjo kwa anthu ena. anthu azikanika kumasuka makomo mwawo chifukwa chatiana timeneti zoona.
"Mmm bambo mwatani kodi? kodi wakambapo zoti anali kukhomo kwamunthu?"
"Ndiye ngati sanali kukhomo kwamunthu mukuganjza ngat wadya k*ti?"
"Mwina nk*theka kusukulu analiko anzake anagula zinthu ndiye anadya nawo? tidziwa bwanji?, tingomudikila kanthawi kena ndimufusitsa". awa anali anambewe kuyankhilapo uku akudzuka pamene anakhala paja

Anachokapo pamalo paja mayiwa ndipo anapita mukhichini ndikukagawa ndiwo za mwana wawo kenako anatenga pelo lawo ulendo wakudilawo kukatunga madzi ndipo anawasiya amuna awo akulimbana ndikafoni kawo kamene k**azima zima.

Aphiri nthawi zambiri amakonda kuvela nkhani nthawi ikakwana 1 koloko ndipo samayiphonya nthawiyi. Mwamwayi kafoni kaja kanayaka ndipo atatsekula Ku wayiresi anazipeza nkhani zikukambidwa.

anava nkhani ina imene inawagwira ntima kwambiri ndipo sanazigwire koma kudzuka ndikuyamba kuvina uku akulankhula avekele...

" Yaah! Boma koma limeneri APA achita bwino k*tsitsa chimanga mwina anthu wovutikafe tizikwanitsako kugula. anavina aphiri uku chimwemwe chitachita kudzadzana pankhope yawo. a linkati movetselabe pawayilesi paka anayamba kukamba zamitengo ya feteleza ndipo apatu foni yawo ija inazimaso.

izitu zinawapweteka chifukwa chidwi chawo chinalo choti ave mene mitengo ya feteleza iliri. anayang'anga kumwamba anawona k*ti kuli mitambo ndikasola kawo sizimagwirizana chifukwa kanali kakang'ono. apatu anapita munyumba ndikukasiya foni yawo ija kenako anatulukamo.

Kukamba za Tamala anali akuweluka kunene kusukulu kuja. sanayiwale kukumana ndi Madam aja ndipo anathokoza kwambiri pazimene anawapangila zija. kukhalaso madam okoma ntima ngati awa Anamuwuzaso Tamala k*ti asamafinyike akawona k*ti njara ikumuwawa aziwadziwitsa. Kenako ntsikana anawatsazika madam ake ndipo anatsazikaso anzake ena kenako anayuwamba ulendo wakunyumba.

Kutengela k*ti kantunda kanalipo ndithu anali akuyenda mwachangu uku akuyimba kanyimbo make kosavetsetseka moti iye anangozindikila wafika kunyumba. Atangofika anaphana maso ndi bambo ake amene panthawiyi anali pantengo wamango kusema mpini. Madala ake chokha chongomuwona anasiya kusema mpini uja ndikuyamba kumuyang'ana koma modabwa.

Anayenda monjanja mwana wankazi ulendo wamunyumba ndipo bambo ake aja sanamufuse. koposa kupitilizabe kusema mpini uja. mwana wankazi anapita kuchipinda kwake kumene anakasintha zovala ndipo atamaliza anatuluka ndikupita kukhichini kumene anakapeza Benja akudya.

Anatenga chakudya chake Tamala ndikuluka panja ndipo anasamba manja kenako anayamba kudya. anangodyako pang'ono chakudya chija kenako chotsalacho anakasiya munyumba kenako anatenga pelo lake ulendo wakudilawo kukatunga madzi. Zosezitu nk*ti madala ake amangoyang'ana ndipo anali wodabwa k*ti anawa chachitika ndichani ndipo anali ndimafuso wosaneneka muntima mwawo amene amasowa mayankho komabe anangozigwira wosafusa.

Alinkati mosema mpini uja Aphiri anangowona kwatulukira nzawo wina amend amagwirizana naye wosati masewela ndipo dzinalake amadziwika k*ti chidothi. Kukamba mosabisa anthuwa amagwirizana kwambiri ndipo anali pachizake chija Amati ponda apa nane mpondepo. Chidothi anali nzawo amene nthawi zambiri amagwilira Nate ganyu limodzi.

Nzawo uja anafika pamene panali iwowo Aphiri uku akulankhula avekele...
"Wawa Aphiri mwagundikatu kunsema mpini azanthu kolowa mwakupeza eti?" .Analankhula Chidothi uku akuseka kupangitsa Aphiri kusiya mpini pasi ndipo anayankha avekele...
"K*k ndipo usakabe moti masana wano ndadyelatu ntchito ndisanagwire moti mpini ndikusemawu ndikukozekela mawa.
" Eee bola azathu ife lero timamaliza kamene tinapeza dzulo moti mene kathelamu mutuso wakula osati masewela.
"Pepa m'bale wanga koma osadandaula ukupeza kolowa zangochitika k*ti tatengelatu tikanati mawa tikagwilire limodzi.
" Zoonadi koma aaa ndine mamuna ndiwona k*ti nditan".Anayankha motelomo nzawo uja ndipo macheza anavumba pamalo paja osati masewela.

Kukamba za nthawi nde inali ikupita ndithu moti inafika nthawi yoti Achidothi aja anatsazika nkumapita kunyumba chifukwa anali atachezapo. kenako Aphiri anadzuka ndikukasiya mpini amasema uja munyumba.

Tamala ndi Amayi ake aja anafika pakhomo paja uku awose ataseza madzi. atatula apatu Anambewe anawayitana amuna awo ndipo sanakhalitse koma anabwela. Tamala analipompo ndipo amayi aja anamuyang'ana Tamala ndipo bambo aja anayamba kulankhula avekele....

IKUPITILIRABE....

Pangani share nkhaniyi kuma group ena k*ti azanuso awelenge nawo💥🔥 ipatseni moto ndima like komaso ma comment anu 💥

😀😂 Benja nde zamuvuta kuyankhatu mwana anachepela K*k Aphiri kusangalal ak*ti chimanga chatsika k**a tikanavako za fetelezaka k*k foni yopoyila. kodi anambewe akufuna kulankhula k*ti chani? zosezi mumpati yotsatila inuyo chofunika ndikupanga like komaso share kuma group k*ti nkhaniyi azanuso awelenge nawo 🔥💥 titipatse moto

wosayiwala kuyika Comment yanu ndimene imandipatsa chilimbikitso k*ti ndizipitiliza kulemba nkhani 🔥💥 yayamba kununkhilatu 😂

wosayiwala kupanga follow page ya simiyon super stories k*ti nkhaniyi isamakuphonyeni

simiyon super stories

= kusangalatsa
= kudziswitsa
= kuphuzitsa

01/10/2025

PALIBE CHOSATHA

PART 2

Wirtten by simiyon mwale

Wosayiwala kupanga follow page ya Simiyon super stories k*ti zambiri zisamakuphonyeni
....

Apatu ntsikana anakokela mpweya ngati akukozekela kumenya mpila ndipo anamezela malovu kenako anayamba kulankhula koma mofoka aveekele......

"Aa madam si, sik*ti ndizimene mukuganizazo ayi, ndikudziwa mukundiganizira molakwika koma sichoncho ayi, zosezi zikuchitika chifukwa cha njala. Dzulo madzulo sitinadye moti tinagona nayo kunyumbaku kulibe kalikose. Apapaso ndikumudela nkhawa nchimwene wanga sindikudziwa k*ti pano akuva bawanji". Analankhula ntsikana koma mofoka kwinaku misozi ik*tsikila masaya mwake

Apatu madam aja anapumila mwamba kwinaku akumuvela chisoni ntsikanayo. kenako anayamba kulankhula madamu aja avekele...
"Wosatandaula Tamala, tiye kunyumba kwanga ukakoze chakudya ineyo ndikamutenga m'ng'ono wakoyo akupeza kunyumba konko. Aaa ndikudziwa mene ukuvela tangopanga zimene ndakuuzazo basi".Anatelo madamu aja uku akudzuka pamene anakhala paja.

Tamala atangova zimenezi anamwetulila uku ak*thokoza kwa madam aja ndipo ananyamuka ulendo wakunyumba kwa madamu akewo. Nawoso madam aja anabwelela mu nkalasi muja kukawatsazika kaye wophuzila aja k*ti akubwela posachedwapa. Kenako anapita ku kalasi imene Benja amaphuzila ndipo atangofika anamwaza maso ndipo sanachite kufusa koma anamuwona Benja amene anali atagona pamene ana anzake wose anali akuphuzila ena kusewela mumadzia inu ana akakhala mu nkalasi.

Apatu anapita pamene panali Benja uja ndikumudzutsa. Atamudzutsa anamutenjela kunyumba kumene anakapeza mulongo wake wagundika kukoza chakudya monga mene anauzidwila. Madam aja sanachedwe koma kubwelela ku school kuja ndipo anangowawuza anawa k*ti ak**aliza awapeza ku school koma anali atawasiyila chilichose chofunikila.

Kukamba za Tamala kakwake kunali k*thokoza basi ndipo anali wosangalara zisanaoneke chifukwa sizimene amayembekezela k*ti zikhoza kuchitika. Atamaliza zose anatenga chakudya chija ndikupita pamene panali ng'ono wake kuja kenako wose anasamba manja ndikuyamba kudya. Alinkati mokudya anawa anayamba kucheza ndipo Benja anayamba kulankhula avekele...

"Eee ndisaname ndinatha moti chipanda madamuwa ndithudi bwezi pano tikukamba zina k*k".Analankhula uku akuseka benja ndipo Tamala anayankhila ali...
"K*k ee njala ndichilombo koma tikuyenela kuwathokozadi madamuwa ndisaname apanga zazikulu. Akanakhala ena akanangotiuza k*ti tizizpita kunyumba ndiye kaya kunyumbako bwezi tikukataniko?. Apapaso nkhawa yayamba kundipeza chifukwa sindikudziwa k*ti kunyumba kuja apanga njila yanji ndikukhulupilira k*ti akungogona ndi njala kumeneku".Anatelo ntsikana uku akudya pamodzi ndi m'bale wake uja.

Atamaliza kudya kuja apatu anawa anatengana ulendo waku school kuja ndipo wose atafika aliyese anapita ku kalasi kwake ndipo Tamala anafika pakhomo ndikugogoda ndipo anapeza Madamu aja akuphuzitsa ndpo anamuuza k*ti atha kulowa. Atangolowa apatu aliyese anali akumuyang'ana modabwa chifukwa samadziwa chimene chimachitika, komaso anali wodabwa k*ti nkhope yantsikanayu imawoneka mosangalala.

Mr Phiri anali akudikila chakudya chimene amaphika akazi awo kwinaku akuvelera tinyimbo kuchokela paka foni kawo koswela chitseko. Mosakhalitsa akazi awo anatulukila uku atanyamula chakudya ndipo atangowona anadzuka mwaphuma ngati chakudya chithawa ndipo amachita kuwona kucheda k*ti madzi wosamba manja bwele chifukwa njala nde inali itawaswa zisanawoneke.

Kenako akazi awo aja anabweletsa madzi aja ndipo mosakhaitsa bambowa anasama manja sanalimbaneso ndikuphemphela koposa kuchiyamba chakudyacho wosadikilaso akazi awo amene ali akusamba manja. Wose anali akudya kwinaku akucheza zinkhani zawo k*tengela k*ti anali ataponyamo nthongo ndiye mau anali atatuluka.

"Eeee zikanavutatu kumene kuja ndisaname ndikanasowa kolowela". Anatelo Mr Phiri uku ak*tema nthongo
"Ndipo simukunama tiwahokoze abwana aja chifukwa chotivetsetsa akanakhala ena sakanatipatsilatu chimanga ganyu tisanagwile..
"kwambiri masikuwano mabwana ngati amenewa akusowa zikufunika ganyu ameneyu akakatipatsa tikagwile mwachangu komaso wadongosolo ndithu".Anatelo awa anali Mr Phiri uk*tu kunali kucheza ndi akazi awi anambewe.

Athawi inali ikupita pang'ono pang'ono ndipo anamaliza kudya kuja. Atamaliza anambewe anatolela mbale ndikusiya kukhichini kenako anapita pamene panali amuna wo ndikupitiliza macheza awo kwinaku akudikila ana awo k*ti abwele kuchokela ku school.

Ali chikhalire anamuona Benja akubwelako uku akuseweletsa mpira wachikulunga zimne zinawadabwitsa makolo aja ndipo anangoti kukamwa yasa wose kuli kusowa cholankhula. Amangoyembekezela k*ti amuwona benja ali wofoka koma ai ndithu mana anali akunjanja ngati kamwana kankhosa. Mafuso wochuluka anali akuzungulira miti yamakokolowa ndipo nkhope zawo wose zinali zitak*tidwa ndikudabwa. Benja anafika pamene panali makolo akewa ndipo Mr Phiri sanachedwe koma kulivumbulutsa fuso avekele....

IKUPITILIRABE....

Pangani share nkhaniyi kuma group ena k*ti azanuso awelenge nawo💥🔥 ipatseni moto ndima like komaso ma comment anu 💥

Kodi a phiri afusa k*ti bwanji?, nanga benja akayankha molondola kodi bambo ake achilamdila motani?, eeee koma kwavuta ineso mafuso akungozungulira mutu mwangamu kodi zik*ta bwabji?...

wosayiwala kupanga follow page ya simiyon super stories k*ti nkhaniyi isamakuphonyeni

simiyon super stories

= kusangalatsa
= kudziswitsa
= kuphuzitsa

30/09/2025

PALIBE CHOSATHA

PART 1

Wirtten by simiyon mwale

Wosayiwala kupanga follow page ya Simiyon super stories k*ti zambiri zisamakuphonyeni

TIYAMBE

Kunja kunali kukucha kumene ndipo kadzuwa kanali kakuwala mwapang'o kuli k*tuluka chapakati kati paphirei lina chakumawa. mbalame zinali zikulira kuphatikizapo zolengedwa zina, uk*tu kunali kunyadila chilengedwe chimene mwiniwake namalenga anachilenga mochititsa chidwi.

Tukamba za anthu nawoso anali ak*tuluka munyumba mwawo ena kumapita kumunda pamene ena anali akupita kuzintchito zosiyana siyana monga mwanthawi zose.

Naloso banja lina linari lik*tuluka munyumba pozindikila k*ti kunja kunali k*tacha, komatu ngakhale limatuluka munyumbamo silinali kusangalala kweni kweni chifukwa chamavuto ena apakhomopo amene amakumana nawo. Banjali linali ndi ana awiri wamamuna ndiwankazi ndipo wamamuna dzina nale anali Benjamini, pamene wankaziyo anali Tamala.

Kukamba za anawa wankulu anali Tamala chifukwa ndamene anayamba kubadwa. Kukamba mosabisa anawa anakula moyo wovutika kwambiri chifukwa cha umphawi wumene unali pakhomo pawo.

"Bambo pamenepa ndikupanga bwanji?, nthawitu ikupita iyi masana wano tikudya chani, tikati tingokhala phee pakhomo pano?". Anaponya mafuso awiri awa anali akazi awo a Mr Phiri kupangitsa k*ti Mr Phiri agwedeze mutu uku akuyang'ana kumwamba ngati k*ti ndikumene kuchokele yankho.
"Mmm kudekhak*tu ndikulingalira k*ti tilowele k*ti, paja nokhaso mukudziwa bwino k*ti maganyu akusowa mudzi muno.
"Ndiye mukuwona k*t nkupanga bwanji pamenepa?". Anapitiliza kuponya mafuso amene amawiritsa mutu wa amuna awo akazi aja.

Kenako Mr Phiri anangodziwa zochokapo pamalo paja uku akugwedezabe mutu wopanda nyanga kuli kusowa ntengo wogwira. Malo moyankha fuso lija anangodziwa zotenga khasu ndik*tola kachipewa kawo ndikuvala. Apatu akazi awo aja anangoti kukamwa yasa, nawoso anapita kukadzutsa ana awo k*ti azipita kusukulu malingana nk*ti dzuwa linali likukwela. Atawawuza ana awo aja iwo anatenga khasu lawo nkuyamba kuwatsatira amuna awo aja ngakhale kumene amapita samakudziwa komabe amangowatsatilabe basi.

Mr Phiri ndi akazi awo analunjika kunyumba ya bwana wina mudelalaro ndipo atafika wose anayima pa gate ndikugogoda. Atapita kanthawi mulonda anatsekula gate lija kenako Mr Phiri anayamba kulankhula avekele...

" Aaa abwana ndawapeza ngati?
" Eya alipo mumawafunila chani?
" Mmm aaa kungot ndimafunako kaganyu kunyumbaku zinthu zandivuta". Analankhula Mr phiri uku akumuyang'ana mulonda uja ndi nkhope yachisoni.
" Ok osadandaula dikilani ndiwafotokozele". Anatelo mulonda uja uku akupita kukawauza abwana aja. Apatu Mr Phiri anamwetulira uku akuwayang'ana akazi awo aja.

Pangopita kanthawi pang'ono kenako abwana aja anafika pamalo paja uku akupuputa manja mwawo kusonyeza k*ti munali madzi. Kenako anawapatsa moni Mr Phiri ndi akazi awo aja.
"Mukhoza kufotokoza chimene mwabwelera". Anatelo abwana aja, apatu Mr Phiri anayamba kufotokoza avekele...

"Aa pepani bwana pokusokonezani komano munthu ine ndi akazi angawa tasowa ntengo wogwira moti kunyumbaku kulibiletu or kachakudya, ndiye timapempha ngati kungapezeke kaganyu bwana k*ti tingopezako kachakudya kalelo". Anatelo Mr Phiri
"Woo ndakuvani Mr Phiri osadandaula, ganyudi alipo wosayamba komano kwalelo ndikuchokapo ndiye mawa muzalawilire mamawa. Aaa apapa ndikupatsani ka 10 kg k*ti mukagaye mukadye lelo". Anatelo bwana aja kupangitsa k*ti Mr phire ayang'ane akazi awo ndinkhope yachimwemwe.

Kenako bwana aja anawauza Mr Phiri pamodzi ndi akazi awo k*ti awatsatile. Apatu wose analowa mumpanda muja ndipo abwana aja anakumana ndi akazi awo ndikuwafotokozela chilichose, ndipo akazi awo aja atava zankhaniyi sananyinyilike koposa kupanga zimene anauzidwa zija. Anakatenga chimanga chija ndikuwapatsa Mr Phiri aja ndipo Mr Phiri sanachede koma kuwauza akazi awo aja k*ti apite kuchigayo akapelesetse.

Pamene amayi aja amapita k*tchini apatu a phri aja anagwana ndikuwathokoza akazi abwana aja kenako ananyamuka ulendo wakunyumba kukadikilira akazi awo aja...

kukamba za ana aja anali atapita ku school ndipo za Tamala anali std 8 pamene benjamini anali std 5. kukamba mosabisa anawa wose anali azelu osati masewela ngakhale amakumana ndizokhoma komano anali ana wolimbikila osati zibana. makolo awo nthawi zose amawalimnikitsa k*ti azilimbikila k*ti mwina k*tsogolo azawagwire dzanja ndipo anawa amalimbikiradi.

tamala anali ali nkalasi ndipo nkhope yake anali atayigoneka pa desk moti zoti anali nkalasi sizimamukhudza. madam anabwela pamene panali ntsikanayu ndipo anamugwila koma akuwoneka wodabwa ndipo anayamba kulankhula avekele...

"Tamala? chavuta ndichani? kapena wadwala?". anafusa mafuso angapo madamu aja ndipo mau amenewa anamututumutsa ntsikanayu zimeneso zinawadabwitsa madamuwa.
"Tamala? ngatitu wadwala utha kumapita ko komaso utha kumuuza nzakoyo akupelekeze kunyumba.
".aaa ayi madam si sik*tiso ndikudwala ayi aaa ku kungoti ndikuwona chizungulire chabe".atangolankhula telo tamala apatu atsikana anzake komaso anyamata amenen anava anamuyang'ana koma modabwa kwambiri chifukwa amaganiza zinana pamene nzawoyo amatanthauza zinaso.

madam aja nawoso anali wsodabwa ndipo sanafune kumupanikiza ndimafuso munkalasimo koposa anamugwila padzanja wose ndik*tuluka panja pamene ndikukakhala pampando ndipo amawonetsa k*ti anali ndimafuso wochuluka madamu aja k*ti avetsetse zimene ak*tanthawuza ntsikanayo. apatu analiponya fuso loyamba madamu aja avekele....

"Tamala? wukati ukuwona chizungulire uk*tanthawuza chani? chonde usandibisile ine ineso ndi munthu wankazi ngati iwe usakhale ndimantha kapena manyazi tafotokoza bwino bwino, aaa komaso undsiuze zimenezo zayamba kuchitika litilo". anawaponya mafuso madam aja mafuso amene pofusa sanamezele malovu, ndipo anatchela mak*tu awo k*ti ave k*ti Tamala ayankha motani komaso afotokoza k*ti chani.

apatu ntsikana anakokela mpweya ngati akukozekela kumenya mpila ndipo anamezela malovu kenako anayamba kulankhula koma mofoka aveekele......

IKUPITILIRABE....

Wosayiwala kupanga share kuma group ena k*ti azanusoawelenge nawo

Tayamba motelo kodi mwayilandila motani?

osayiwala kupanga follow page ya simiyon super stories k*ti nkhaniyi isamakuphonyeni

simiyon super stories

= kusangalatsa
= kudziswitsa
= kuphuzitsa

Address

Kasungu

Telephone

+265982550349

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Simiyon super stories posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share

Category