27/10/2025
ποΈ 27 Oct 2025
Kadzutsa wa Mau; ULENDO OWERENGA BIBLE
π Yoswa 7:1-26
*Lingaliro*
Mavuto samatha ndi kulira! Kugonja ndi "mwayi" odzifufuza ndi kukonza chomwe chalakwika. Kulephera kutero ndi tsoka; minyama yeniyeni.
ππ _palemba_
19. Ndipo Yoswa anati kwa Akani, Mwana wanga, uchitiretu ulemu Yehova Mulungu wa Israyeli, numlemekeze Iye; nundiuze tsopano, wachitanji? usandibisire.
20. Ndipo Akani anayankha...
21. pamene ndinaona pazofunkha maraya abwino a ku Babulo, ndi masekeli mazana awiri a siliva, ndi chikute chagolidi, kulemera kwake masekeli makumi asanu, ndinazikhumbira ndi kuzitenga; ndipo taonani, ndazibisa m'nthaka pakati pa hema wanga, ndi siliva pansi pakepo.
Nkhani ya Akani ili ndi maphunziro ozama. Nawa ena mwa iwo:
1. Mulungu amalora anthu osachimwa afe "kunkhondo" ndipo ochimwa apulumuke, powapatsa mwayi olapa tchimo lao. Akani wakubayo anapulumuka, pomwe ankhondo 36 anafa!
2. Tchimo limaumitsa mtima kuti munthu asamve chidzudzulo. "Tilipo ambiri," amadzilimbitsa mtima, osadziwa chiweruzo ndi cha aliyense payekha. "Mudzipatule..." koma Akani sanatero; sanadziwe kuti mwayi wake unali ukutha pang'ono-pang'ono.
3. Kusekerera tchimo, m'malo modzudzula, kumasandutsa anthu kukhala othandizira tchimo (accomplices) ndipo amayenera kugawana nao zotsatira za tchimolo. Apabanja la Akani ankadziwa za katundu yemwe anabayo chotero anafa naye pamodzi.
4. Tchimo limasowetsa mtendere. Akani anafa "atabisa chuma" m'malo mochidyerera!
_"Ndipo Yoswa anati, Watisautsiranji? Yehova adzakusautsa lero lino. Ndipo, Aisrayeli onse anamponya miyala, nawatentha ndi moto..." (v 25)_
Tsoka la Akani litipatse ife lero nzeru. Amen