Frank Dines

Frank Dines Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Frank Dines, Grocers, Frank, Lilongwe.

17/05/2024

Wachiwiri kwa wa pampando wa komiti wa masapota a timu ya FOMO m'chigawo chapakati, Peter Malata, ali kuchipatala komwe akulandira thandizo pomwe wavulazidwa ndi anthu ena omwe akuganiziridwa kuti ndiotsatira timu ya Creck Sporting.

Malingana ndi mlembi wa mkulu wa komiti ya masapota a FOMO kuchigawo chapakati, Felix Guga, wati anthu oganiziridwawa anafika pa bwalo la Civo kudzachita zomwe akukhulupilira kuti ndizazikhulupiliro zawo pamapeto pazokonzekera za timu ya FOMO.

Koma atakanizidwa kulowa mu bwalo la zamaseweroli, anthuwa adayamba kumenya wachitetezo wa FOMO komanso Malata ndipo mwa mwayi wachitetezoyi adathawa pomwe Malata wavulazidwa, ndipo adatengeredwa kuchipatala komwe akulandira thandizo.

Tinayesera kuti tiyankhule ndi mlembi wamkulu wa timu ya Creck Sporting, Aaron Mtaya, koma anati timuimbire pakapita ola imodzi chifukwa choti ali pansewu.

Tikhala tikukupatsirani zambiri

Ras Peter Kansengwa wafika ku India komwe akuyembekereka kulandira thandizo la chipatala pa vuto lake la miyendo.Pa kuch...
24/04/2024

Ras Peter Kansengwa wafika ku India komwe akuyembekereka kulandira thandizo la chipatala pa vuto lake la miyendo.

Pa kucheza kwathu kudzera pa lamya Kansengwa anafotokoza kuti wafika bwino ndipo zonse zili m'chimake kuti athandizike.

"Nditangofika tsabata latha ndisaname anandilandira bwino mwa msangala, ayi ndithu ndinamva kamphepo kena konyaditsa, chikhulupiliro chilipo kuti zonse zikhala mbambande,"iye anatero akusekelera.

Anapitilira kunena kuti padakali pano madotolo ali kalikiliki kuyeza zina ndi zina nthupi asanapitilire ndi ntchito yonse yomwe ikuyembekezereka ndipo nthawi yomaliza dongosolo yonse idziwika madotolo akamaliza zoyezayeza.

Tikuyankhula naye Kansengwa pa lamya amamveka wachimwemwe chodzadza tsaya ngati kuti sakudwala moti tinapezerapo mwayi kumfusa kuti "Zisankho zomwe zili mkati ku India anthu akuti bwanji"

Sanazengereze koma kuyankha ndi mphamvu kuti "mwachita bwino kufunsa, anthu avota kwa masabata asanu ndi imodzi, zisankho zizalengezedwa pakazatha masiku atatu kuchokera tsiku lomamaliza ku vota."

Anaonjezera kuti zipani zotsutsa zapanga m'gwirizano kuti mwina zingagonjetse a Narendra Modi omwe ndi a Prime Minister olamula apano a chipani cha Bharatiya Janata Party (BJP).

Kansengwa anatsiliza ndikuthokoza onse amene amuthandiza ku uzimu komanso ku thupi kuti zonse zitheke.

"Mulungu adalitse Boma la Malawi komanso a Malawi onse," iye adatero.

Wolemba: Manson Msukwa

BREAKNEWSPatapita masiku ochepa timu ya mighty mukulu wanderers itabweresa osewera wakutsogolo wa ziko la Cameroon zatsi...
23/04/2024

BREAKNEWS

Patapita masiku ochepa timu ya mighty mukulu wanderers itabweresa osewera wakutsogolo wa ziko la Cameroon zatsikimizika tsopano timuyi yathekesa chili chonse ndi timu ya (Mkokala fc) ya dziko la zambia pa osewera wawo wakumbuyo (Jackson Ibrahim) wazaka 22 zakubadwa malingana ndi malipoti owe zikumveka timuyi ikhala ikusayina osewera awili kumathelo asabata ino

21/04/2024
HUMBA AKUFUNA 50 MILLION KWACHA NGATI CHIPEPESO KUCHOKA KU BOMA KAMBA KOMANGWIDWA Wapampando wa komiti yoyendetsa masewe...
08/04/2024

HUMBA AKUFUNA 50 MILLION KWACHA NGATI CHIPEPESO KUCHOKA KU BOMA KAMBA KOMANGWIDWA
Wapampando wa komiti yoyendetsa masewero chigawo chakummwera Raphael Humba wasumira boma kuti limupatse ndalama zokwana 50 million kwacha kamba ka kumangidwa pankhani yabodza.

Humba anamangidwa mmbuyomu powaganizira kuti amagwiritsa ntchito pepala (certificate) ya fomu 4 yomwe imkaganiziridwa kuti mwini wake anamwalira.

Malingana ndi kalata yomwe yasainilidwa ndi Gilbert Khonyongwa, woimira mlandu a Humba wati ndalamazi akufuna apatsidwe kamba koti mbiri yake inawongeka komanso ankamuyendetsa akudwala.

Mdandaulo lawo Khonyongwa wati a polisi anafika mpakana kupita ndi Humba kumanda posakasaka kuti apeze amene akuti ndi 'Raphael Humba

MATCHDAY      ONE(TNM Super League)Mighty Mukuru Wanderers FC vs Kamuzu Barracks Date: Sunday,7th  April 2024Venue: Kamu...
07/04/2024

MATCHDAY ONE
(TNM Super League)

Mighty Mukuru Wanderers FC vs Kamuzu Barracks

Date: Sunday,7th April 2024
Venue: Kamuzu Stadium
Charges: K3,000 open stand,K4,000 MBC,K5,000 Covered and K7,000 VIP
Time: 14:30hrs

New replica Jersey ikhala mawa ikugulitsidwa Ku stadium🤍💙🐜🐜🐜zimayenda ngat msomba
06/04/2024

New replica Jersey ikhala mawa ikugulitsidwa Ku stadium🤍💙🐜🐜🐜zimayenda ngat msomba

Leading at the break - let's build on this, Gunners 👊
06/04/2024

Leading at the break - let's build on this, Gunners 👊

Mene zathera lero
06/04/2024

Mene zathera lero

Basitu pa Dedza tangotenga galimoto yomwe makaka ake akuoneka ngati a tnm aja basi kuti kulomcha kusavute. ___Komatu awa...
06/04/2024

Basitu pa Dedza tangotenga galimoto yomwe makaka ake akuoneka ngati a tnm aja basi kuti kulomcha kusavute.

___Komatu awawa akupwetekana kaya mukuona

Address

Frank
Lilongwe

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Frank Dines posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share

Category