Grace 2 sadzu

Grace 2 sadzu you are welcome to my page, feel free to ask and read πŸ“š my stories
(4)

Pali m'tsikana wina yemwe anatuluka mu m'tsinje atavala tawelo ndipo anandiuza kuti akufuna asambe nane .Part 2 ...........
04/09/2026

Pali m'tsikana wina yemwe anatuluka mu m'tsinje atavala tawelo ndipo anandiuza kuti akufuna asambe nane .

Part 2 ........

Ndinamuuza m'tsikana ameneyi kuti ndikuyenela ndikaganize kaye chifukwa aka kanali koyamba kumuona .

Ndinayamba kuzifunsa ndekha kuti m'tsikana ameneyi angakhale ndani nanga mmadzimu amapangamo chani.
Apa ndinaganiza kuti pali chinsinsi chachikulu chomwe chimachitika mmudzi mwathu mwa ngomani .

Nditafika kunyumba mtima wanga unayamba kugunda kwambiiri ndipo mtendele unandisowa. Ndinaganiza zoti ndimuuze mzanga yemwe anali ku town.
Ndinatenga phone πŸ“± yanga ndayamba kulemba message ku WhatsApp.

" hello nzanga RAJABU, 1 hour yapitayi ndinali ku m'tsinje ndipo ndakumana ndi m'tsikana yemwe amandiuza kuti ndisambe naye komaso anavala towel ya white ndipo anandiuzaso kuti amandikonda .
Ndinatero pa message paja

Rajabu anayankha nati "

Usadandaule Daniel, umenewu ndi mwanayi wako , ukudziwa kale atsikana akumudzi amakonda amuna oti angobwela kumene kuchokera ku town.
Iweyo usakane ndipo upange naye zachikondi, sindikuona chinthu choti chochititsa mantha .

Noooo ndili ndi mantha . M'tsikana ameneyi anatuluka mmadzi ndikuona ngati simunthu weni weni.
Ndinamuyankha chomcho Rajabu.

Ndipo nayeso adayamba nati kwa ine .
M'tsikana ameneyi nkutheka kuti anachita kulowa mmadzi iweyo usanafike . Nkutheka kuti amasambila ndiye iweyo usaope .mawa upite ukasambe naye .
Adatero Rajabu.

Sindinawauze amayi anga nkhani imeneyi chifukwa ndinkaopa kuti mwina andiuza miyambi yoopsa kwambiiri ya mmudzi mmenemo.

Tsiku lotsatilari ndinapita ku m'tsinje kuja ,anthu ena analiso kumtsinje komweko koma osati malo omwe ineyo ndinakhala .

M'tsikana uja anatuluka mmadzi muja ndipo anabwela pafupi ndi ineyo nayamba kulankhula .

Kodi waganiza kale zomwe ndinakupempha zija kuti tisambile limodzi?
Adafunsa m'tsikana uja ndipo ineyo sindinayankhe .

Adandigwila nkono nayamba kupitiliza kulankhula.

Kodi mnyumba waku town iwe, ndikhulupilira kuti waganiza bwino pempho lomwe ndinakuuza lija .
Tiyeni tilowe mmadzi kuti tonse tisambile limodzi basi .

Adatero m'tsikana uja kwinaku atavala tawelo yake ya white.

Naneso ndinamugwila dzanja ndipo tinapita pamalo aziii mu m'tsinje muja ndipo chodabwitsa china chinachitika ndithu ......

Ikupitilirabe.........

03/09/2026

Apa tazitoleraso ndithu

Part 1....Pali mzimayi wina yemwe anatuluka mu m'tsinje atavala tawelo ndipo anandiuza kuti akufuna asambe nane. Dzina l...
03/09/2026

Part 1....

Pali mzimayi wina yemwe anatuluka mu m'tsinje atavala tawelo ndipo anandiuza kuti akufuna asambe nane.

Dzina langa ndine Daniel. Tsiku lina ndinaganiza zopita kumudzi kwathu kuti ndikaone nyumba yanga yomwe ndinkamangitsa panthawi yomwe ndinali kutawuni .

Mudzi wakwathu umatchedwa Ngomani ndipo unkatchuka kwambiiri ndi ulimi wansomba komaso chimanga .

Mudzi umenewu unali ndi mitsinje komaso nyanja zokongola .madzi adali ponseponse ndipo unali mudzi odalitsika .

Tsiku lina ndinapita kumtsinje waukulu kuti ndikachape zovala zanga zakuda .
Ndili nkati mochapa ndinamva nkokomo wamadzi ndipo mwachangu changu ndinayimilira kuti ndionetsetse chomwe chikuchitika.

Posakhalitsa ndinaona pakati pa m'tsinje patayamba kubwata ngati kuti madzi akubwatila pamoto .

Mulungu wanga ine !!!
Ndinadzidzimuka . Ndipo panthawi yomweyi ndinaona m'tsikana okongola kwambiiri yemwe anatuluka pamadzi . Adavala tawelo ya white .

Ndipo ndinaganiza zoti ndithawe koma m'tsikana uja anandiuza kuti ndisathawe .

Kenako adandiyandikila pafupi . Koma thupi lake linali lokuda ngati makala koma adali m'tsikana okongola ndithu.

Usandiope komaso usathawe chonde , ineyo sindingapange choipa kwa iweyo .adatero m'tsikana uja .

Kenako adasunthila pafupi kwambiiri ndiineyo kwinaku akupukuta kumaso kwake ndi tawelo ija. Timano take tinali tokongola komaso toyela bwino ngati madzi a mpunga .

M'tsikana uja anayamba kulankhula mawu kwa ine nati ;

Iwe Daniel, ndakhala ndikungokuona nthawi yonse umachapayi ngakhale ndinali mmadzimu.
Komano ndikufunitsitsa titasambila limodzi iweyo ndiineyo " adatero m'tsikana uja "

Wanena kuti chani ? Ineyo sindingachite zimenezi komaso ndichifukwa chani iweyo watiluka mmadzi ngati nsomba? Ndiwe chiwanda kapena?
Ndinamufunsa m'tsikana uja ndipo iye anayankha nati ;

Siine nsomba ndipo ndine munthu ngati iweyo. Ndikufunitsitsa nditasamba nawe kenako ndikhale wachikondi wako .kodi nditchimo kupanga chibwenzi ndi mnyamata ooneka bwino ngati iweyo?

M'tsikana uja adandifunsa ndipo naneso ndinayankha motere.

Ndidikile kaye ndikaganize ndipo ndikuyankha mawa pazomwe wanenazi .
Ndinamuyamkha chomcho

Mtima wanga unkagunda, ndipo ndinayamba kulingalira muntima mwanga .

Kodi ndikuwe ? Mmm koma mwina anthu sangandimve .kodi nditati ndathawa atha kuuluka ndikundigwila ?

Apatu ndinayamba kulingalira Mozama kwambiiri kuti ndipezele njila yothawila . Kunena chilungamo ndinali ndi nkhawa

Ndinapakila zovala zanga mu basin kuti ndidzipita kunyumba.

Ubweleso mawa ndidzakupatsa yankho leni leni.
Ndinamuuza choncho m'tsikana uja ndipo iye adangomwetulira ulendo obwelera komwe adachokela .

Ndinapita kunyumba koma ndili ndi mkhawa komaso mafunso.

Kunena chilungamo ndi m'tsikana okongola .

Kodi ndivomele kusamba naye ?
Komano kodi angakhale ndani ?

Awa anali mafunso omwe ndinali nawo mumtima mwanga .

Ikupitilirabe..........

ambiri mukulota ndikudziwa , ndiye ine ndimafuna ndivunge maunis koma nonse mukuliza nkonono
02/09/2026

ambiri mukulota ndikudziwa , ndiye ine ndimafuna ndivunge maunis koma nonse mukuliza nkonono

Bwelani mupange DNA mwaulele ndi Doctor Grace. azibambo Sendelani pafupi
24/08/2026

Bwelani mupange DNA mwaulele ndi Doctor Grace.

azibambo Sendelani pafupi

mukamvera nyumba ya rent mundiuze mwamvq
20/08/2026

mukamvera nyumba ya rent mundiuze mwamvq

kod mwagona kale ?
14/08/2026

kod mwagona kale ?

30/07/2026

eti muli inuyo mungatan ? koma mwaswera bwanji, tilipo ndithu kungot tikuthawa abahambe

27/07/2026

Good night guys πŸšΆβ€β™€οΈπŸšΆβ€β™€οΈπŸšΆβ€β™€οΈπŸšΆβ€β™€οΈ

17/07/2026

kukhala opanda data ndi mbola , zambiri zikuchitika ndithu mm

Address

Cape Town

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Grace 2 sadzu posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to Grace 2 sadzu:

Shortcuts

Share

Category